Wapolisi wavulala, kulandidwa mfuti ku Kasungu

Wapolisi wavulala, kulandidwa mfuti ku Kasungu

Wa polisi m'modzi wavulala pa chiphwilikiti chomwe chinabuka pa mudzi wa  Ganthu  kwa mfumu Kayesa mdera la mfumu Lukwa ku Kasungu usiku walachinayi.

Anthu a mmudziwo akuti analanda mfuti pa chipolowecho, chomwe akuti chinadza kaamba koti munthu wina akufuna kuti awasamutse pa mudzipo kuti atsekulepo munda.

Mfumu Kayesa yati anthuwa anakwiya ndi kubwera kwa apolisi pa mudzipo, pa nkhani yomwe akuona kuti akuphwanyilidwa ufulu wawo.

"Mudzi wa Ganthu udayamba mchaka cha 1932, koma m’modzi mwa akubanja la chifumu akufuna abale ake , asuweni asamuke kuti azilimapo zomwe mzolakwika," inatero mfumuyi.

Koma mneneri wa apolisi ku Kasungu a Josephy Kachikho wati nthambi ya za nkhalango inakatenga apolisiwo kuti akathandize kulanda makala ndipo ndi komwe chiphwilikiticho chinabuka.

Iwo atsimikiza za kuvalazidwa kwa wapolisiyo, ndipo anati apolisi akufufuza kuti adziwe msonga yeniyeni ya nkhaniyi.

"Ofesi ya za nkhalango inatifunsa kuti akufuna asilikali kuti akalande makala. Ngati anthuwo akuti ndi nkhani ya malo ndiye kuti tifufuza," atero a Kachikho.

Wapolisi yemwe wavulalazidwa ali mchipatala cha Kasungu ndipo mfuti yomwe anthuwo analanda yapezeka.

Read 1089 times

Last modified on Friday, 11/08/2023

Login to post comments
Go to top
JSN Time 2 is designed by JoomlaShine.com | powered by JSN Sun Framework