A Chilima Alowa M’manda Lolemba; UTM Ikufuna Mayankho
Mwambo wachitika wotumiza kwao matupi a ena mwa anthu omwe adafa pa ngozi ya ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa purezidenti wa dziko lino Lolemba.
Mwambowu inatsogolera ndi nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ku nyumba ya chisoni ya Sunset ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.
Panali akuluakulu apolisi ndi asilikali, malinga n’kuti ena mwa anthuwa anali a zachitetezo.
Ena mwa awa ndi awa:
- A Lukas Kapheni, omwe kwao ndi ku Kasungu, omwe amagwira ntchito ku polisi ngati wachitetezo ndi zothandizira a Chilima.
- A Daniel Kanyemba, omwe anali dotolo wapadera wa a Chilima ndipo kwao ndi kwa a Chiseka ku Lilongwe.
- Major Flora Selemani Gwirinji, omwe amayendetsa ndege ndipo amagwira ntchito ku MDF; kwao ku Thyolo.
- Colonel Owen Sambalopa, othandiza kuulutsa ndege, omwe kwao ndi ku Malosa, Zomba.
- A Chisomo Chimaneni, omwe amagwira ntchito ku polisi komanso anali wotsogolera achitetezo a Chilima.
- Major Wales Aidini, omwe anakali makaniki wa ndege, omwe kwao ku Nankumba, Mangochi.
Thupi a Shanil Dzimbiri, omwe anali mkazi wakale wa mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Bakili Muluzi, aliyika m’manda kwawo ku Balaka Lachisanu.
Prezidenti Lazarus Chakwera anali nawo pa mwambo wonyamula thupi la a Dzimbiri, pomwe a Muluzi anali ndi akuluakulu a boma ambiri.
Thupi la a Abdul Lapukeni, mmodzi wa omwe anafa limodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino pangozi ya ndegeyi Lolemba aliika mmanda kwawo ku Mangochi Lachitatu. Iwo anali wachiwiri kwa mkulu owona zochitika mu ofes ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko.
Nduna yoona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena a Nancy Tembo, omwe anayimira a Prezidenti Chakwera ku mwambowu, anati a Lapukeni anali munthu okhulupirika pa ntchito komanso okonda dziko lake.
Malinga ndi a Kunkuyu, thupi la a Chilima aliyika m’manda kwao ku Nsipe m’boma Ntcheu Lolemba.
Lachisanu ndi Loweruka anthu apereka ulemu otsiriza kwa a Chilima ku nyumba ya malamulo ya boma ku Area 12 Lilongwe, komwe kuli siwa. Lamulungu kudzakhala mwambo wa dziko lino ku bwalo la za masewero la Bingu ku Lilongwe.
Kupempha Chilungamo
Chipani cha UTM, chomwe a Chilima amatsogolera, chapempha kuti pakhale kafukufuku wapadera kudzera ku nthambi yoyima payokha yowona za ngozi za ndege.
Icho chati izi zithandiza kupeza chomwe chachititsa ngoziyi komanso kudzetsa imfa.
Polankhuala kwa atolankhani ku Lilongwe, mlembi wamkulu wachipanichi, a Patricia Kaliati, wati chiyembekezo chawo n’choti kafukufukuyu akamukhazikitsa adzapereka zotsatira zomwe zidzapereka chikhulupiliro kwa aMalawi.
Mwazina, a Kaliati ali ndi nkhawa kuti panatenga nthawi yaitali kuti opulumutsa anzawo pa ngozi ayambe kusaka malo omwe ndegeyi inagwera, komanso akuganiza kuti anthu ena sanauze Prezidenti Chakwera zoona.
Koma polankhula pa msonkhano wa atolankhani Lachitatu, a Kunkuyu anati nthambi ya gulu la nkhondo la MDF ichita kafukufuku wake wapadera.
A Kunkuyu ati ntchito yofufuza gwero la ngozi ya ndege yomwe yapha a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu ichitika ndi nthambi zomwe zakonzeka kutero.
Major General Syford Kalisha, m’modzi wa akuluakulu a nthambiyi naye watsimikiza izi, ponena kuti kufufuzaku atenga masiku khumi.
Mlowa M’malo
Katswiri wa za malamulo a Justice Dzonzi wati n’koyenera kuti Prezidenti Lazarus Chakwera asankhe wachiwiri wake watsopano mwamsanga popewa kuti ofesiyi ikhale yopanda munthu kwa nthawi yaitali.
A Dzonzi ati ngakhale malamulo a dziko lino sapereka nthawi yomwe angatenge asanasankhe mlowa mmalo, n’kofunika kusankha munthu pa udindowu mu nthawi yoyenera.
Malamulo a dziko lino amapereka mphamvu kwa prezidenti zosankha wachiwiri wake watsopano ngati yemwe anali pa udindo wamwalira, watula pansi udindo komanso kulephera kugwira ntchito pa zifukwa zina.
Phunziro
Katswiri wa zokhudza mtendere ndi chitukuko wati imfa yadzidzi ya wachiwiri kwa mtsogoreli wadziko lino komanso zolepheretsa zomwe zinalipo posaka malo omwe ngoziyi inachitikira zichititse boma kugula zipangizo zoyenera zomwe zingathandize nthawi za ngozi.
A Master Mfune, omwe amayankhulanso pa nkhani zachitetezo, ati zipangizo zoterezi, monga ndege za mtundu wa helikopika komanso tindege tating’ono towuluka pogwiritsa ntchito kompyuta (ma droni), zitha kuthandiza kwambiri kupulumutsa miyoyo pa ngozi
Akatswiri ena a zandale ati imfa ya a Chilima ikhudza kwambiri ndale komanso chitukuko cha dziko lino.
A George Chaima ndi a Ernest Thindwa ati Dr Chilima anathandizila kwambiri posintha momwe achinyamata amaonera ndale komanso kuchititsa kuti ambiri atenge nawo mbali pandale mdziko lino.
A Chaima atinso a Chilima alowa m’mbiri ya dziko lino kaamba koti anali ofunikira kwambiri pothandiza chipani cha MCP kuti chilowenso m’boma patatha zaka zochuluka chikulephera kutero kudzera pa chisankho.
Last modified on Friday, 14/06/2024