Standard Bank - BOL to Wallet

Sankhani Wachiwiri Motsata Lamulo – Mabungwe

Kondowe; popanga chiganizochi a Chakwera asagonjere maganizo a anthu Kondowe; popanga chiganizochi a Chakwera asagonjere maganizo a anthu

Bungwe la National Advocacy Platform (NAP) lapempha mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera kuti alemekeze malamulo posankha wachiwiri wake mu nthayi yoyikika.

Wapampando wa bungweli a Benedicto Kondowe wapemphaso mtsogoleriyu kuti asankhe munthu amene amakonda dziko kuti athandize anthu m’dziko muno kudutsa munyengo yowawa yokhuza imfa ya a Chilima.

Koma a Kondowe ati popanga chiganizochi a Chakwera asagonjere maganizo a anthu ena omwe akufuna kukwaniritsa zolinga zawo pa ndale.

Mamulo a dziko lino amati mtsogoleri wa dziko ayenera kusankha wachiwiri wake watsopano ngati yemwe analipo wamwalira kapena akulephera kugwira ntchito pa zifukwa zina m’masiku asanu ndi awiri.

M’mau ake, mtsogoleri wa bungwe lamaloya, Malawi Law Society, a Patrick Mpaka wati n’kofinika kuti mtsogoleriyu alemekeze malamulo posankha m’lowa m’malo wa malemu Chilima kuti ntchito za boma zisaime.

“Mwachitsanzo, pa mndandanda wa nduna za boma pamayenera kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko. Ngati palibe, ndiye kuti lamulo laphwanyidwa,” iwo anatero.

Ngati malamulo angatsatidwe, a Chakwera amayenera kulengeza munthu yemwe alowe m'malo mwa malemu Chilima ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzulo lisanathe tsiku la Lachitatu pa 19 June.

M’kalata ya posachedwa, bungwe la maloyali lati malinga ndi imfa ya a Chilima, a Chakwera akuyenera kusankha mlowa m'malo pasanadutse pa 19 June.

A Mpaka atiuza kuti ngakhale malamulo sanafotokoze chomwe chingachitike ngati prezidenti satsatira izi, malamulo akutsindika kuti m’njira iliyonse akuyenera asankhe wachiwiri wake, ndithu.

Poyamba, boma linati aMalawi ayembekezere kuti Prezidenti Chakwera asankha munthu wolowa m'malo mwa a Chilima ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko malinga ndi zomwe malamaulo a dziko lino amakamba.

Nduna yoona zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu yauza atolankhani Lachiwiri ku Lilongwe kuti a Chakwera ndi mtsogoleri wolemekeza komanso kutsatira malamulo.

Ofesiyi ilibe munthu potsatira imfa ya a Chilima Lolemba sabata yatha pa ngozi ya ndege.

A Kunkuyu ati zokambirana zayamba ndi akadaulo a mayiko akunja kuti adziwe chomwe chinachititsa ngozi ya ndege yomwe idapha a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu. Ndegeyo inagwera mu nkhalango ya Chikangawa.

A Kunkuyu ati kafukufukuyu akhudza ukadaulo wa momwe ndege inalili komanso zomwe zidachitika isanawuluke ndinso pambuyo pa kuyamba ulendo wake.

Padakali pano, akuluakulu achipani cha UTM ati akonza zokumana kumapeto a sabata ino kuti akambirane za momwe chipanichi chipitilire patsogolo potsatira imfa ya a Chilima.

Malinga ndi mneneri wa chipanichi, a Felix Njawala, akhala akukumana pafupipafupi kuti awonetsetse kuti asunga owatsatira komanso kuteteza masomphenya a mtsogoleri wawo.

Thipi la a Chilima linalowa m’manda ku mudzi kwawo, Mbirimtengerenji, ku Nsipe ku Ntcheu, Lolemba pamwambo omwe panali a Chakwera ndi atsogoleri ena ambiri.

Read 7014 times

Last modified on Wednesday, 19/06/2024

Login to post comments
Go to top
JSN Time 2 is designed by JoomlaShine.com | powered by JSN Sun Framework