Msonkhano Waukulu wa PDP Ulipo pa 13-14 September
Chipani cha Peoples Development (PDP) chati chidzachititsa msonkhano wake waukulu pa ku Blantyre kuyambira pa 13 mpaka 14 September, ndipo anthu akapikisana pa mipando yonse kuphatikizapo wa mtsogoleri.
Mneneri wa chipanichi a Rhodes Msonkho walengeza izi pa msonkhano wa atolankhani omwe anachitsa ku Lilongwe Lachiwiri.
A Msonkho ati aika K1.5 million ngati ndalama yoti okapikisana pa udindo wa mtsogoleri wa chipani apereke ndi K1.3 million pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri.
Iwo ati aika ndalama zochepa kuti ofuna kupikisana apereke pofuna kuti anthu ambiri, maka achinyamata ndi amai, akwanitse kupereka.
“Ndalamazi ndizochepa kuyerezeka ndi zomwe zipani zina zaika. Ena, monga a mipando a m’musi adzireka K300, 000 yokha,” anatero a Msonkho. “Ndalamazi ntchito yake ndikuthandiza chabe kuti msonkhano waukulu uyende bwino, osati kupeza phindu.”
Iwo ati aliyense atha kupikisana pa mpando uliwonse – mamembala akale komanso omwe akulowa kumene chipanichi.
Chipani cha PDP anachikhazikitsa ndi a Kondwani Nankhumwa, omwe anali mtsogoleri wa zipani zotsutsa m’nyumba ya malamulo, atawachotsa m’chipani cha DPP.
Last modified on Tuesday, 06/08/2024