Owaganizira Kupha Awamanga
Apolisi amanga abambo atatu - a Gift Banda a zaka 29, a Yusuf Matola a zaka 33 ndi a Regan Phiri a zaka 39 - powaganizira kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa mzika ya dziko la South Korea pa 7 February chaka chino.
Mzikayo, a Woonja Hwang, inaphedwa pafupi ndi mtsinje wa Lilongwe pomwe imapita kukaphunzira masewero a tenisi ku bwalo la Lilongwe Golf Club.
Anthuwa akuwaganiziranso kuti anaba lamya ya m’manja ya malemuwo.
Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m'dziko lino Superintendent Alfred Chimthere watiuza kuti anthuwa akaonekera m’bwalo la milandu posachedwapa, kukayankha mlandu wokupha.
Last modified on Wednesday, 13/03/2024