Apolisi Amanga Woganiziridwa Kutaya Mwana
Apolisi kwa Ngabu m'boma la Chikwawa amanga mai wa zaka 20, Maria Akimu, pomuganizira kuti anataya khanda lake lobadwa kumene usiku wa Lachiwiri.
Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m'bomalo, Consitabo Chance Mfune, wati Akimu anathawa atapalamula mlanduwu.
Iye wati apolisi agwira Akimu Lachisanu anthu ena atawatsina khutu za komwe anali.
Maria Akimu ndi ophunzira pa sukulu ya sekondale m'deralo.
Khandalo analitaya m’chimbudzi.
Bambo yemwe amakhala moyandikana ndi msungwanayo akuti anamva khanda likulira m’chimbudzi, ndipo anauza anthu ena omwe anathandizira kulipulumutsa.
Achitapatala adati mwanayo, yemwe ndi wamwamuna, anali kupeza bwino.
A Mfune ati msungwanayo, yemwe amachokera m'mudzi mwa Mwadula m'dera la mfumu yaikulu Ngabu, ayankha mlandu obisa uchembere.