Lerani Ana a Khungu la Chialubino Monga Winaliyense – Massa

Massa Massa - wojambula George Kalungwe

Womenyera ufulu wachibadwidwe, a Boniface Massa, walangiza makolo omwe ali ndi ana akhungu la chialubino kuti adziwapatsa thandizo lonse loyenera kuti akule n’kudzakhala mzika zodalirika.

Iwo anauza anthu ku Lilongwe pa nkhomaliro yomwe anakonzera anthu a khungu la chialubino, makolo awo ndi anansi kuti iwo anafika pomwe ali lero chifukwa makolo awo anawawonetsera chikondi.

A Massa ndi m’modzi wa makomishonala a bungwe la boma loteteza ufulu wa anthu, Malawi Human Rights Commission, ndinso mkulu wabungwe la Standing Voice Malawi lomwe iwo anayambitsa.

“Tinaganiza zokonza nkhomaliro imeneyi kuti tikhale limodzi ndi kusangalala ndi anzathu a khungu la chialubino lero pamene ndi tsiku lokumbukira za ulumali pa dziko lonse,” anatero a Massa, “Atithandiza kukonza phwandoli ndi a hotelo ya Lucky One chifukwa amaona zomwe timachita.”

A Mussa anati ana a ulumali akalandira thandizo loyenera amakula monga mwana wina aliyense, amakhala odzikhulupilira ndipo amachita bwino pa maphunziro, zomwe zimawathandiza kudzakhala mzika yodalirika.

Nkhomaliro yomwe a Massa akakonza inachitika pa tsiku lomwe linali lokumbukira ufulu wa anthu a ulumali pa dziko lonse, pa 3 December, lomwe linakhazikitsa bungwe la mgwirizano wa maiko onse, United Nations.

A Jessie Chiyamwaka, mkulu owona zophunzitsa anthu nkhani za ulumali mu nthambi yowona za ulumali ndi achikulire mu unduna wa zachisamaliro cha anthu anati mwambowo unali ofunika kwambiri.

“Mwaona apa, kupatula kudyera limodzi, anthuwa akuphunzitsana momwe angasamalilire matupi awo, kulera ana ndi zina zambiri. Zimenezi ndi zofunika kwambiri. Pali madotolo pano omwe akupereka uphungu ofunika,” iwo anatero.

Hotelo ya Lucky One inathandiza popereka chakudya, malo ndi zinthu zina mwaulele.

Malinga ndi a Patrick Thoko Banda, mkulu owona za malonda ndi zofalitsa nkhani ku hoteloyi, nthawi yakwana yoti kampani nazo ziyambe kuteteza ufulu wa anthu aulumali.

Iwo anati akukhulupilira kuti thandizo lawo lilimbikitsa ufulu wa anthu omwe ali ndi khungu la achialubino.

Read 406 times
Login to post comments
Go to top
JSN Time 2 is designed by JoomlaShine.com | powered by JSN Sun Framework