Mai Wazaka 23 Akuthawa Mwana Onyentchera ku Neno

Mwa zina, anthu aku Neno asonkha ndalama zokwa K140 thousand ndipo zagula katundu monga mafuta ophikira Mwa zina, anthu aku Neno asonkha ndalama zokwa K140 thousand ndipo zagula katundu monga mafuta ophikira - chithunzi ojambula ndi Steve Kalungwe

Mkulu wa ofesi ya chisamaliro cha anthu m'boma la Neno a Paul Sosono wachenjeza makolo omwe amathawa udindo wawo kuti adzalandira chilango chokhwima kutsatira zomwe mai wina wazaka 23 akuchita pomathawa mwana wake wazaka zisanu yemwe tsopano wanyetchera.

Mai ake a mwanayu a Veregina Katekedza wauza Zodiak Online lero kuti iwo amachita izi kamba ka umphawi ndipo amapezeka m'malo omwera mowa ku Mwanza komanso m'dziko la Mozambique poti amuna awo anawathawa ndipo amasowa chisamaliro.

"N’zoona ndimamuthawadi. Komatu ndine osauka ndipo amuna anga anandithawa choncho ndimasowa chisamaliro. Komabe ndisintha izi sizizachitikanso," watero maiyu.

Mwanayu yemwe pansinkhu wake sakwanitsa kudya payekha komanso kuyenda, amakhala nthawi zambiri ndi agogo ake omwe iwo atinso zinthu zimawavuta.

A Sosono ati ngati njira yofuna kusamalira mwanayu, tsono amuika mugawo lochita nawo mafizo komanso adzilandira chiponde pa chipatala cha Neno zitadziwikanso kuti mwanayu alinso ndi mavuto ena kamba kolekeleledwa.

"Sitinafune kugwiritsa ntchito lamulo pazomwe maiwa akuchita, tikufuna kupereka mpaka oti asinthe kamba koti tawapatsa uphungu oyenera," anatero a Sosono.

Mkulu wa bungwe la Beyond Our Hearts Foundation a Russel Msiska omwe anasonkhetsa ndalama zothandizira kugula zofunika pamoyo wamwana, wati makolo adzitenga udindo osamalira anawo osati kusiyira ena.

Mwa zina, anthu aku Neno asonkha ndalama zokwa K140 thousand ndipo zagula katundu monga mafuta ophikira, ndiwo (mazira, soya pieces) chimanga, mbaula, ziwiya zophikila mwazina.

Mkulu wa mapulani ndi chitukuko pa khonsolo ya Boma la Neno a Charles Lomoni anati ndiwodabwa ndi zomwe mai Veregina Katekedza akuchita polekelera mwana.

"Ndine wamantha ndi khalidweli, chipatala chili pafupi ndi muno m'mudzi mwa Nkhuku-Zalira, pompa apa mpaka mwana kufika saizi iyi? Anatero a Lomoni.

Komabe iwo ati ngati izi zitapitilire kufala m'boma la Neno, amema adindo kuti adzipereka chilango.

A Esnart Macheka omwe ndi mkulu wa ofesi yakadyedwe kabwino pa chipatala cha Neno anati mwanayu anafikapo pa chipatalachi pa 2 January chaka chino ndipo anamutulutsa pa 17 mwezi omweuno.

Iwo ati izi "nkamba koti pa nsikhu wake, malinganso ndi mfundo za umoyo, mwanayu sali oyenera kupitiliza kukhala kumafizo komabe chiponde tikumpatsa komanso amayenderedwa ndi azaumoyo".

Mkulu wa police ya Neno a Edwin Magalasi nawo anati " izi nzonvetsa chisoni ndipo bambo wamwanayu akuyenera naye apezeke ayankhepo".

Boma la Neno ndilimodzi mwa maboma omwe nkhani zonyetchera zili patsogolo ndi 45 percent.

Read 707 times
Login to post comments
Go to top
JSN Time 2 is designed by JoomlaShine.com | powered by JSN Sun Framework