Odwala Akufunika Chakudya Chabwino - Chiponda

Odwala Akufunika Chakudya Chabwino - Chiponda

Unduna wa zaumoyo wapempha nthambi za boma zomwe zikuchita ulimi pansi pa ndondomeko ya minda ikuluikulu ya ulimi wa bizinesi kuti zizidzipereka zina mwa zokolola zawo ku zipatala za boma kuti odwala adzidya chakudya chabwino ndi chopatsa nthanzi.

Nduna ya zaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda imalankhula Lachitatu ku Lilongwe pomwe unduna zachilengedwe umapereka matani 1.85 a nsomba za ndalama zokwana K7.9 million ku chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe.

Iwo ati thandizoli ladza mu nthawi yabwino chifukwa lithandiza odwala omwe amafunika chakudya chapadera chopatsa nthanzi.

“Odwala, monga omwe avulala pa ngozi ya moto amafuna chakudya cha mavitamini monga nsomba kuti khungu libwerere,” anatero a Kandondo Chiponda.

Iwo anati nthambi za boma zomwe zikuchita ulimi wa bizinesi zidzipatulako zokolora zawo ndikupereka ku zipatala zazikulu za boma komanso za m’maboma.

“Inu monga a MDF [asilikali], a ndende ndi ena, tikukupemphani kuti mukakolora zina mudzitha kutithandizirako kuti tidzipereka kwa odwala. Kuno kumakhala anthu ena osowa abale, omwe amafuna thandizo la chakudya.

“Komanso amalonda; ukamudutsa mu Lizulumu [ku Ntcheu] umatha kuona tomato akungowonongeka, mbatatesi ndi masamba... Ndimaganiza kuti nditangokhala ndi 2 tanu [lore], n’kutenga tomato amene uja kubwera naye kuno. Mukawona kuti izi simutha kugulitsa, bwanji mudzitapatsa,” inapempha chotero ndunayi.

A Kandondo Chiponda anati anamwino ndi madotolo omwe amathandiza odwala usiku adzidya nayo nsombazo.

“Koma chonde osatengako kupititsa kunyumba, ayi. Ndisamve zimenezo. Mudziphikira komwe kuno. Odwala kumadya; inunso kudya basi. Tikudziwa m’magwira ntchito yolemetsa.”

Polankhula kwa atolankhani, nduna ya zachilengedwe, a Michael Usi, inati imamvetsa bwino zakufunika kwa chakudya chopatsa nthanzi kwa odwala.

Iwo anati, "Tapereka thandizo limeneli ku chipatala cha Kamuzu lero pofuna kulimbikitsa moyo wa nthanzi pakati pa odwala. Kudya moyenera kumathandiza kuti munthu achire msanga.”

"Nsomba zomwe tikuperekazi tazigwira mu Nyanja ya Malawi. Eni ake ndi aMalawi. Tikulingalira zothandizanzo zipatala zina,” anatero a Usi “Sindinena kuti ku Blantyre kaya Mzuzu tipita liti, koma ndife okonzeka ndithu kuthandiza.”

Thandizoli alipereka kudzera ku nthambi ya zakafukufuku ya unduna wa zachilengedwe ndi kusintha kwa nyengo yomwe ili ku Monkey Bay m’boma la Mangochi.

“Timagwira nsomba pamane tikupanga kafukufuku. Nthawi zina timatha kuzibwezera m’madzi kapena kutaya, koma ulendo uno tinaganiza kuti tiziwambe ndi kuzikonza mwapadera kuti tidzapereka kuno ku chipatala,” anatero m’modzi wa akuluakulu owona zakafukufuku ku nthambiyo, a James John Banda.

Zina mwa nsomba zomwe apereka ndi Sawasawa, Kampango, Bombe ndi Ndunduma.

Read 772 times

Last modified on Thursday, 14/09/2023

Login to post comments
Go to top
JSN Time 2 is designed by JoomlaShine.com | powered by JSN Sun Framework