Anthu Awapempha Kuti Adzikonda Makanema Achimalawi

Okonza mwambo wa chionetsero cha makanema cha chaka cha 2024 (Malawi Film Festival) adandaula kuti anthu ochepa akhala akubwera ku mwambowu ndipo apempha aMalawi kuti adziyamikira luso la m’dziko muno osati kukonda mafilimu akunja okha ayi.

Yemwe amayendetsa mwambowu, a Phillip Kuipa Phiri, wati n’zokhumudwitsa kuti anthu ochepa amapezekapo pamwambowu womwe udachitika kuyambira Lachisanu mpaka Loweruka ku Lilongwe ngakhale kuti okonza, bungwe la Film Association of Malawi, adayesetsa kumemeza anthu.

A Kuipa Phiri adati ngakhale zili zovomerezeka kuti ntchito zopanga makanema m’Malawi muno sizidatukuke, kupezeka kwa aMalawi ambiri pamwambowu kutha kulimbikitsa okonza makanena a m’dziko muno kuti adzipanga mafilimu opatsa chidwi.

“Zitha kutanthauza zambiri. Mwina anthu saakonda mafilimu a md’ziko muno kapena ife, ngati akonza mwambowu, sitinafalitsa uthenga kwa anthu ochuluka kuti abwere. Koma ndikudziwa akuti aMalawi amakonda makanema awo; n’zosangalatsa kuwonera filimu yomwe zomwe zikuchitikamo ukuzidziwa,” iwo anatero, polenjeza kuti chaka cha mawa adzatchukitsa mwambowu kwambiri.

Mwa ena, katswiri wakale malemu Hope Chisanu wadalandira mphotho ya Munthu Wochita Zakupsya M’moyo Wake pomwe Innocent Manyera ndi Mada Kafamtenga adalandira mphoto monga mwamuna ndi mkazi ochita zisudzo bwino kuposa onse mu 2024.

Kanema yabwino ya pa televishioni ndi Dear Ex; pomwe nkhani yopambana pa kanema ndi The Devil in Me. 

ZODIAK ONLINE

ArtBridge House, Area 47
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Text: (265) 999-566-711
support@zodiakmalawi.com

Information

Quick Links

Follow Us

Login

{loadmoduleid ? string:16 ?}