Thupi la Papa Lilowa M’manda Loweruka

Likulu la mpingo wa Katolika, Vatican, lalengeza kuti mwambo wa maliro a Papa Fransis uchitika Loweruka nthawi ya 10 koloko m’mawa.

Nyumba yofalitsa nkhani ya Reuters yatsimikizira za chikonzerochi.

Malinga ndi uthenga wachidule omwe atulutsa, mwambo wa malirowu ku St Peter Square udzayundetse ndi Cardinal Giovanni Battista Re, mkulu wa bungwe la ma Kadinolo. 

Pambuyo pa mwambowu, bokosi lake adzapita nalo ku Basilica ya St Peter, kenako ku nyumba Santa Maria Maggiore kuti akalike m'manda.

Padakali pano atsogoleri a dziko lapansi akupitiriza kulingalira za moyo wa Papayu.

Mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera, wati ndiwokhudzidwa ndi imfayi potengera kuti miyezi ingapo yapitayo anakumana ndi mtsogoleriyu.

Bungwe la mabishopu a mpingo wa Katolika m’dziko lino lagwirizana ndi mpingo yonse padziko lonse pokhuza imfa ya mtsogoleriyu.

Wapampando wabungweli Bishop Martin Mtumbuka wapempha aKhristu ampingowu kuti apempherere mzimu wa Papa Francis.

Padakali pano, mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera wati ndiokhudzidwa ndi imfayi potengera kuti miyezi ingapo yapitayo anakumana ndi mtsogoleriyu.

 

ZODIAK ONLINE

ArtBridge House, Area 47
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Text: (265) 999-566-711
support@zodiakmalawi.com

Information

Quick Links

Follow Us

Login

{loadmoduleid ? string:? string:16 ? ?}