A Chakwera Achotsa Gawo Lina la Uthenga Wawo; Katswiri wati N'zamanyazi

A Chakwera kuyankha mafunso m'nyumba ya malamulo

Pulezidenti Lazarus Chakwera wachotsa gawo lina la uthenga wake ku mtundu wa aMalawi pa momwe zinthu zikuyendera m’dziko muno omwe anapereka m’nyumba ya malamulo pa 14 Febuluwale 2025, zinthu zomwe sizinachitikepo m’mbiri ya Malawi.

Izi zachitika dzulo potsatira kuchuluka kwa kusankhutira kwa aphungu otsutsa ndi anthu ena pa zomwe a Chakwera analankhula m’nyumbayi, zomwe ena anati unali uthenga wokopa anthu pokonzekera chisankho cha mu Seputembala.

Poyankhula poyankha mafunso a aphungu, a Chakwera adati achotsa gawo lina la zomwe analankhula ndinso kuchotsa mtsogoleri wa gulu la akatswiri asanu lomwe linapereka uthenga wa zomwe analankhula m’nyumbayi.

Koma, Pulezidenti Chakwera wati anthu omwe akutsutsa uthenga onse omwe adapereka mnyumbayi safunira dziko lino zabwino, ndipo akungofuna kukwanilitsa zolinga zawo la ndale, zomwe iye sangagonjere.

Uwu unali uthenga omwe mtsogoleri wa dziko amapereka kwa aMalawi kudzera m’nyumba ya malamulo poyamba pa chaka chatsopano cha zokambirana za aphungu.

Uthengawu unalinso wotsiriza wa mtundu wotere kwa a Chakwera m’ndime yawo yoyamba ya zaka zisanu za utsogoleri wa dziko pamene akukonzekera kuyimanso kachiwiri pa chisankho cha pa 16 Sepitembala 2025.

Mwazina, zinapezeka kuti mu uthengawu a Chakwera anafotokoza ntchito zina za chitukuko, monga nyumba za ogwira ntchito zachitetetezo, kuti zatsirizika, koma chonsecho zisanayambe n’komwe.

Zodiak inapeza akuti pali umboni ochokera m’maboma 16 woti zina mwa zomwe a Chakwera analankhula ndi zosiyana ndi momwe zinthu zikuyendera.

Mtsogoleri wa zokambirana m’nyumba ya malamulo, a Richard Chimwendo Banda, adalankhula ndi atolankhani potsimikizira zomwe mtsogoleri wa dzikolinoyu wachita, ponena kuti cholinga chake n’kuwonetsa ugwiro wake.

“Apulezidenti achita izi posonyeza ugwiro. Limenelo ndiye lamulo, timati pali zina zomwe zimachotsedwa, ndipo zina zimavomerezedwa. Iwo akuti sangaime pa chinthu chomwe sichoona,” anatero a Chimwendo Banda.

Koma ndunayi yadzudzula aphungu otsutsa chifukwa chonyanyala msonkhano omwe pulezidenti anali nawo ndi aphungu kuti ayankhe mafunso awo pa uthengawo wakewo.

“Izi ndi zochititsa manyazi. M’mbiri ya dziko lino sichinatikepo aphungu otsutsa kuthawa m’nyumba ya malamulo kutabwera mtsogoleri wa dziko. Zoona aphungu otsutsa kulephera kukonza mafunso opita kwa pulezidenti?”

Nthawi yomwe pulezidenti amalankhula nyumba ya malamulo dzulo, aphungu otsutsa adanyanyala ndi kutuluka.

Pamsonkhano wa atolankhani womwe adachititsa, mtsogoleri wa zipani zotsutsa, a George Chaponda, ananenetsa kuti a Chakwera achotseretu uthenga wawo onse komanso kuti usalowe m’buku la mbiri ya zochitika m’nyumbayi, Hansard, m’Chingerezi.

“Tikuti uthengawu ndiwosagwirizana ndi malamulo a dziko lino; awuchotseretu wonse. Iwo anasankha kulankhula zinthu za bodza, m’malo mofotokozera aMalawi momwe zinthu zachuma, chakudya...zikuyendera.”

Zachilendo

Zinthu zingapo zachilendo zinachitika m’nyumba ya malamulo Lachitatu pa 26 Febuluwale 2025, monga Purezidenti kuchotsa gawo lina la uthenga wake, omwe m’Chingerezi mwachidule amati SONA, ndi kuchotsa pa udindo nduna polankhula kwa aphungu.

Nduna yomwe ayichotsa ndi a Sosten Gwengwe, omwe m’malo mwawo mwalowa a Vitumbiko Mumba ku unduna wa zamalonda ndi mafakitale.

Kuwachotsa a Gwendwe  kwadza pamene aMalawi ali ndi nkhawa ndi kukwera udyo kwa mitengo ya zinthu.

A Peter Dimba tsopano ndi nduna ya zantchito, kulowa m’malo mwa a Mumba, ndipo wachiwiri kwa nduna yowona za mtengatenga ndi ntchito ndi a Steven Malondera, omwe alowa m’malo mwa a Dimba omwe awakweza paudindo.

Katswiri wa zandale a Chimwemwe Tsitsi wati zomwe zachitikazi ndi zochititsa manyazi.

A Tsitsi n’zomveka kuti a Chaponda akufuna kuti uthenga wonse wa a Chakwera asawuwerengere chifukwa izi ndi koyamba kuchitika m’mbiri ya dziko lino.

ZODIAK ONLINE

ArtBridge House, Area 47
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Text: (265) 999-566-711
support@zodiakmalawi.com

Information

Quick Links

Follow Us

Login

{loadmoduleid ? string:? string:16 ? ?}