ZODIAK ONLINE
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Nzika ya dziko lino Jacqueline Msiska Bokosi ali nawo mgulu la anthu ochita ntchito zamalonda padziko lonse omwe alandira nawo mphoto zomwe apereka a Global Recognition Awards chaka chino.
Kalata yomwe opereka mphotozi atulutsa yati a Bokosi ndi amasomphenya, odziwa za utsogoleri komanso ulimbika pa ntchito za chitukuko chamakono ndi za luso.
Majaji omwe apereka mphothoyi ati anagoma ndi nkhani ya mayiyu, kuti posatengera zokhoma zomwe wakumana nazo wakwanitsa kudzutsa bizinezi yapamwamba yomwe ikukula mwachangu.
A Bokosi alandira mphothoyi kamba kokhala mayi wa luntha, komanso momwe amayendetsera bizinezi yawo ya CTS Courier.
"Kuwunika bwino zomwe a Bokosi a chita, tapeza kuti akwanilitsa zambiri, komanso amafikira zomwe makasitomala awo akufuna," yatero kalatayo.
Kampani ya CTS yomwe a Bokosi anakhazikitsa, ndiyodalilika pa ntchito za mtengatenga. Iwo ali ndi nthambi 30 m'dziko lino.
Mayi Bokosi apambana kale mphotho zitatu chaka chino komanso atchulidwa nawo ngati m'modzi mwa anthu amene atha kupambana nawo Consumer Choice Awards.