ZODIAK ONLINE
Sect. 5, P/Bag 312
Lilongwe, Malawi
Pamene nthawi imati 6 koloko mmawa Lachiwiri, malo ambiri oponyera voti anali atawatsekula pa chisankho cha pulezidenti, aphungu, ndi makhansala.
Ngakhale m'madera ambiri voti inayamba bwino, kwina zinthu zinachedwa chifukwa cha vuto la makina ndi kakonzedwe ka mizere.
Mwachitsanzo, ku Kasungu mtolankhani wathu Wilson Allan Phiri anacheza ndi a Gerald Chirwa omwe ndi mkulu wa bungwe la National Innitiative for Civic Education (NICE) kumeneko.
Iwo anati ndiwokhutira ndi momwe chisankho chikuyendera ngakhale kuti panali vuto loti kuponya voti kunayamba mochedwa ngakhale kuti anthu anafika nthawi yabwino mmawa.
Mtolankhani wathu Nobert Tambalamtuwa Mzembe anali pamalo oponyera voti a Kavuzi, komwe anati zonse zinayenda bwino zomwezo yemwe akutsogolera ntchito yoyendetsa chisankho voti pamalowa a Chancy Kondowe anatsimikiza.
Ku Blantyre ntchito yoponya voti inayamba yayima kwa maola oposera atatu pa malo ena.
Mtolankhani wathu kumeneko Chikondi Mphande wati ntchito yovota inayima pomwe anthu ena amanena kuti awona ma pepala ena ochonga kale koma akuluakulu a MEC atsutsa izi.
Malinga ndi wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja ati mapepala ena oponyera voti anagwera inki.
Kupita ku Dedza, maka pa ndende ya Dedza, mtolankhani wathu Ernest Gama anacheza ndi yemwe akuyang'anira pamalowa a Ruth Chigwenembe, omwe ati akayidi ena asanu sanaponye voti kaamba koti mayina awo sanapezeke.
Anthu 284 ndi omwe analembetsa pa ndendeyi.
Abambo awiri omwe anabwera kudzaponya voti pa malo oponyera voti pa sukulu ya pulaimale ya Namaka m'boma la Chiradzulu makina ozindikira ovota (Biometric) anakanika kuzindikira zidindo za chala chawo cha mkomba phala (finger print).
Mmodzi wa akulu akulu omwe akuyang’anira pa malowa a Holiness Mponela auza mtolankhani wathu Elijah Phompho kuti pena izi zimatha kuchitika kaamba ka ntchito zina zomwe anthu amagwira monga kupala matabwa kapena kulima zomwe zimatha kufufuta zidindo za m'manja ndi zala.
"Abambowa tinawalolabe kuponya voti kaamba koti maina awo anapezeka m'buku la mkaundula wa ovota koma tikumalimbikitsa anthu kusamba m'manja ndi sopo akafika pa malowa ngati njira imodzi yoti zala zizizindikirika mosavuta," anatero a Mponela.
Ku Ntchisi, A Innocent Luka, omwe akuyang'anira kumeneko afotokoza kuti kuponya voti kunayambika patadutsa mphindi makumi atatu (30) kaamba zovuta zina.
"Pa chifukwa ichi, malowa tiwatseka nthawi ya 4:30 osati 4 koloko monga momwe bungwe la MEC lidanenera," Atero a Luka.
Ku Mzuzu, maka pa malo oponyera voti a sukulu ya Nkhokwe, ntchito yoponya voti inayima kwa mphindi 15 kaamba ka kusamvana komwe kunalipo pakati pa anthu omwe amafuna kuvota pa malopa ngakhale analibe kalata zosamukira.
"Anthuwa tinawabwenza ndipo sanaponye voti chifukwa analibe kalata za transfer," atero a Endita Mumba, omwe akuyang'anira pamalowa.
Ntchito yoponya voti anapitilira, kudutsa 4:30 pm m'madera osiyanasiyana omwe inachedwa kuyamba.
Omwe akupikisana kwambiri pa chisankho cha pulezidenti ndi mtsogoleri wa padakali pano a Lazarus Chakwera (MCP) ndi mtsogoleri wakale a Peter Mutharika (DPP).
(By Racheal Julaye)